TIDIKIRE MPAKA AYAKE - CHIFUKWA IZI NDIYE NDI KHWESI


 Anthu  ambiri ochita malonda anali kakasi kaamba ka kuzima kwa magetsi komwe kunachitika masana a lachiwiri  pa 9 July.

Vuto la kuzima kwa magetsili  linasokoneza ntchito zamalonda, maka zomwe zimadalira magetsi mmadera ambiri m'boma la Lilongwe.

Mwachitsazo, pa msika waung'ono  wa Matindi, achinyamata omwe amachita bizinezi yometa anthu komanso kutchaja mafoni adandaula kuti vuto la kuzima kwa magetsili lasokoneza kwambiri ntchito zawo lero.

 Nawo amayi omwe amafuna kukagayitsa, anali khumakhuma mmakonde a zigayo kudikira kuti mwina magetsiwa  ayaka.

Ndipotu ngakhale kuti kunja kunali kutada, Nathenje Community Radio inapeza amayi ochuluka omwe anali  akudikirabe  mmakonde azigayozi poganiza kuti mwina magetsiwa ayaka.

Ndipo patatha maola oposa asanu ndi limodzi kuchokera pomwe magetsiwa athima, Magetsi anayaka. 

Chomwe chinachititsa kuti magetsiwa azime motere sichikudziwika pakali pano.

Wolemba: Enerst M Manyoni

Comments

Popular posts from this blog

AFTER DEADLY PROTESTS, KENYANS TELL OF BRUTAL ABDUCTIONS

AONESA CHIDWI CHODZAPIKISANA NAWO NGATI KHASALA