AONESA CHIDWI CHODZAPIKISANA NAWO NGATI KHASALA
Modzi mwa achinyamata okhala pa Nathenje Gift Mkochi watsimikiza kuti ayimira nawo ngati Khasala wa Ngala Ward pachisankho chomwe chichitike chaka cha mawa dziko muno.
a Mkochi ati akufuna kudzapikisana nawo pa chisankhochi atawona kuti kwanthawi yayitali Ngala Ward yatsalira Ku nkhani ya chitukuko.
"Inetu ndi mwana wamudzi muno, ndaphunzira konkuno ndipo zanga zonse zili kuno. Ndi zokhumudwitsa kuti ntchito ya Khasala kwathu kuno sikudziwika!!! Ndikufuna anthu adziwe kuti Khasala amatani" anayakhula motero a Mkochi
Iwoso atsimikiza kuti akonzeka kukathamangitsana ndi anzawo ena kumasankho achipulura a chipani cha Malawi Kongelesi mwezi wa seputembala uno
Wolemba: Alinafe Jonasi & Loveness Chiutsi
Chithunzi: Shadow Khasala Gift Mkochi
Comments
Post a Comment