TIDIKIRE MPAKA AYAKE - CHIFUKWA IZI NDIYE NDI KHWESI

Anthu ambiri ochita malonda anali kakasi kaamba ka kuzima kwa magetsi komwe kunachitika masana a lachiwiri pa 9 July. Vuto la kuzima kwa magetsili linasokoneza ntchito zamalonda, maka zomwe zimadalira magetsi mmadera ambiri m'boma la Lilongwe. Mwachitsazo, pa msika waung'ono wa Matindi, achinyamata omwe amachita bizinezi yometa anthu komanso kutchaja mafoni adandaula kuti vuto la kuzima kwa magetsili lasokoneza kwambiri ntchito zawo lero. Nawo amayi omwe amafuna kukagayitsa, anali khumakhuma mmakonde a zigayo kudikira kuti mwina magetsiwa ayaka. Ndipotu ngakhale kuti kunja kunali kutada, Nathenje Community Radio inapeza amayi ochuluka omwe anali akudikirabe mmakonde azigayozi poganiza kuti mwina magetsiwa ayaka. Ndipo patatha maola oposa asanu ndi limodzi kuchokera pomwe magetsiwa athima, Magetsi anayaka. Chomwe chinachititsa kuti magetsiwa azime motere sichikudziwika pakali pano. Wolemba: Enerst M Manyoni